Bungwe la NASFAM lati ndilokukhutira ndi momwe alimi m’boma la Nkhotakota alandirira komanso kugwiritsa ntchito uphungu wokhudza kasamalidwe ka zokolola, kuyambira kumunda mpaka kumsika, womwe ukuperekedwa kudzera mu pulojekitiyi.
Polankhula atangocheza ndi alimi komanso alangizi a
zaulimi m’bomali, mlangizi wa NASFAM, Frank Masankha, wati bungweli lipitiliza
kulimbikitsa njira zabwino zaulimi, kuonetsetsa kuti pakhale chakudya
chokwanira komanso kupititsa patsogolo luso la alimi posamalira zokolola.

Masankha: Ndife okhutira kwambiri
Masankha wati: “Monga NASFAM, ndife okhutira kwambiri.
Taona alimi akugwiritsa ntchito uphungu umene akulandira, ngakhale kuti panali
mavuto ena m’madera ena.”
Masankha watsimikiziranso alimi m’bomali kuti
pulojekitiyi, yomwe yakhala ikugwira ntchito kwa miyezi isanu, ipitilira ndipo
ifikira alimi ambiri.
M’modzi mwa alimi omwe Umunthu FM inacheza nawo, Lyson
Banda wa ku Linga EPA, wati pulojekitiyi yathandiza alimi kudziwa zambiri,
makamaka za mmene angasamalire zokolola akafika nazo kunyumba, ubwino wogwirira
ntchito limodzi ngati banja zotsatira za kusasamalira bwino mbewu, zomwe
zingapangitse kuti mbewu zikhale ndi chiopsezo cha chikukhodzo chomwe chimatha
kuyambitsa matenda a khansa.
Banda wati: “Ife ngati alimi tinakondwera kuti bungweli
linapereka njinga zamoto kwa alangizi a m’madera, pofuna kuti azifikira madera
akutali ndi uphungu wofunikawu.”
Komabe, Banda wati pali mavuto ena omwe akukumana nawo,
kuphatikizapo kuchepa kwa chiwerengero cha alimi omwe alembetsedwa
m’ndondomekoyi, kusowa kwa misika yodalirika komanso kusowa kwa matapulini
m’madera ena.
Bungwe la NASFAM, mothandizidwa ndi ndalama kuchokera ku
AGRA, linakhazikitsa pulojekiti ya Regain m’maboma a Nkhotakota, Mchinji,
Lilongwe ndi Mzimba, ndi cholinga chochepetsa kuwonongeka kwa zokolola.