NASFAM ikhutira ndi momwe pulojekiti ya Regain ikuyendera m’boma la Nkhotakota
Bungwe la NASFAM lati ndilokukhutira ndi momwe alimi m’boma la Nkhotakota alandirira komanso kugwiritsa ntchito uphungu wokhudza kasamalidwe ka zokolola, kuyambira kumunda mpaka kumsika, womwe ukuperekedwa kudzera mu pulojekitiyi. Polankhula atangocheza ndi alimi komanso alangizi a zaulimi...