Breaking:
Nkhotakota flood victims raise sanitation fears as government moves to prevent cholera-/-Green Skills Training Key to Environmental Protection
National Sep 21, 2026 02:28 PM Tapiwa Mbewe

NASFAM ikhutira ndi momwe pulojekiti ya Regain ikuyendera m’boma la Nkhotakota

NASFAM ikhutira ndi momwe pulojekiti ya Regain ikuyendera m’boma la Nkhotakota
Chithunzi: Tsiku loyendera alimi

Bungwe la NASFAM lati ndilokukhutira ndi momwe alimi m’boma la Nkhotakota alandirira komanso kugwiritsa ntchito uphungu wokhudza kasamalidwe ka zokolola, kuyambira kumunda mpaka kumsika, womwe ukuperekedwa kudzera mu pulojekitiyi.

Polankhula atangocheza ndi alimi komanso alangizi a zaulimi m’bomali, mlangizi wa NASFAM, Frank Masankha, wati bungweli lipitiliza kulimbikitsa njira zabwino zaulimi, kuonetsetsa kuti pakhale chakudya chokwanira komanso kupititsa patsogolo luso la alimi posamalira zokolola.

Masankha: Ndife okhutira kwambiri

Masankha wati: “Monga NASFAM, ndife okhutira kwambiri. Taona alimi akugwiritsa ntchito uphungu umene akulandira, ngakhale kuti panali mavuto ena m’madera ena.”

Masankha watsimikiziranso alimi m’bomali kuti pulojekitiyi, yomwe yakhala ikugwira ntchito kwa miyezi isanu, ipitilira ndipo ifikira alimi ambiri.

M’modzi mwa alimi omwe Umunthu FM inacheza nawo, Lyson Banda wa ku Linga EPA, wati pulojekitiyi yathandiza alimi kudziwa zambiri, makamaka za mmene angasamalire zokolola akafika nazo kunyumba, ubwino wogwirira ntchito limodzi ngati banja zotsatira za kusasamalira bwino mbewu, zomwe zingapangitse kuti mbewu zikhale ndi chiopsezo cha chikukhodzo chomwe chimatha kuyambitsa matenda a khansa.

Banda wati: “Ife ngati alimi tinakondwera kuti bungweli linapereka njinga zamoto kwa alangizi a m’madera, pofuna kuti azifikira madera akutali ndi uphungu wofunikawu.”

Komabe, Banda wati pali mavuto ena omwe akukumana nawo, kuphatikizapo kuchepa kwa chiwerengero cha alimi omwe alembetsedwa m’ndondomekoyi, kusowa kwa misika yodalirika komanso kusowa kwa matapulini m’madera ena.

Bungwe la NASFAM, mothandizidwa ndi ndalama kuchokera ku AGRA, linakhazikitsa pulojekiti ya Regain m’maboma a Nkhotakota, Mchinji, Lilongwe ndi Mzimba, ndi cholinga chochepetsa kuwonongeka kwa zokolola.

Leave a Comment
Comments (0)
    Live Streaming
    Live Radio Stream
    đź”´ LIVE 00:00